Salima District Council

Salima District Council Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Salima District Council, Government Organization, Salima.

Khonsolo ya Salima yapereka pulojekiti yomanga mdadada wasukulu ya Katawa CDSS ndi nyumba imodzi ya aphunzitsi kwa konti...
26/09/2026

Khonsolo ya Salima yapereka pulojekiti yomanga mdadada wasukulu ya Katawa CDSS ndi nyumba imodzi ya aphunzitsi kwa kontirakita wa Urban Engineering kuchigawo chapakati chakumadzulo kwa boma la Salima.

Pulojekitiyi yomwe ili pansi pa thumba la ndalama la 5 billion Reformed Constituency Development Fund ndiya ndalama zoposera 440 million ndipo ikuyembekezeka kugwiridwa kwa masiku okwana 90.

Poyankhulapo, Phungu wanyumba yamalamulo wakuderaku, Enock Phale wati ndiwokondwa ndichitukukochi chifukwa ndizimene anthu amafuna.

Iye wati ndiwodzipereka kugwira ntchitoyi mwachangu ndipo wapempha Khonsolo ya Salima kuti izichita changu popereka zonse zoyenera kuti ntchitoyi isachedwe.

Phale walimbikitsa makontirakitala kuti agwire ntchiyoyi mwaukadaulo ndikumanga chinthu cholimba.

Sub TA Kanzimbe wati Sukuluyi ithandizira kuchepetsa maukwati a ana pomwe ambiri amasiira sukulu panjira kamba koyenda mtunda wautali popita kusukulu.

Mlangizi wamkulu owona zakusasiyana pakati pa amayi ndi abambo, anyamata ndi atsikana Friness Samaliya wauza makontirakitala kuti asatsekere amayi kunja polemba anthu ntchito.

Iye wati pa anthu 10 aliwonse olembedwa pakuyenera kukhala akazi 4 kupita m'mwamba.

Iwo adafotokozanso kuti anthu akuyenera kulandira malipiro awo mu nthawi yoyenera ndipo ntchito yomanga siyikuyenera kugwiritsa ntchito njerwa zowotcha koma za simenti, pofuna kusamalira chilengedwe.

Wapampando wa gulu la Mtukulapakhomo ku Ntchentche, dera la Mfumu Kalonga ku Salima, Fletcha Mbumba, wapempha boma kuti ...
25/09/2026

Wapampando wa gulu la Mtukulapakhomo ku Ntchentche, dera la Mfumu Kalonga ku Salima, Fletcha Mbumba, wapempha boma kuti anthu a m’madera adzatenge nawo mbali posankha omwe akuyenera kupindula, popewa kuyika anthu osayenera mundondomekoyi.

Mbumba walankhula izi kutsatira kusintha komwe kulipo pa kayendetsedwe ka mtukula pakhomo, pomwe anthu ena akuyembekezereka kuchotsedwa mu ndondomekoyi.

M'modzi mwa akulu akulu mu unduna wowona kuti palibe kusiyana pakati pa amuna ndi akazi, yemwe amayang'anira ntchito yosankha anthu mundondomekoyi Anastazio Matewere, wanena kuti pulogalamu ya Mtukulapakhomo ikusintha chifukwa cha kuchepa kwa thandizo la ndalama kuchokera kwa mayiko ndi mabungwe omwe amathandizira.

Matewere wafotokoza kuti chiwerengero cha opindula chichepetsedwa kuchoka pa 381,000 kufika pa 108,000 dziko lonse la Malawi, pomwe ku Salima chichepetsedwa kuchoka pa 11,814 kufika pa 3,368, kuyambira Januware 2027 mpaka 2029.

Iye wati komabe, ndalama zomwe banja lililonse lidzalandire zikukwera kuchoka pa K16,850 kufika pa K32,040–K41,000, malinga ndi kukula kwa banja lopindula.

Senior Group Kalonga yayamikira boma chifukwa cha pulogalamuyi, ponena kuti yathandiza kusintha miyoyo ya anthu, komaso walimbikitsa opindula kuti azigwira ntchito molimbika kuti athe kudzidalira.

Mmodzi mwa opindula, Jessie Benitala, wayamika thandizoli, ponena kuti lamuthandiza kugula zinthu zofunika kwa ana a sukulu komanso kugula mbuzi.

Pakadali pano, akulu akulu alimbikitsa omwe apitilize kupindula kuti azigwiritsa ntchito ndalamazi mwanzeru.

24/09/2026

Salima DC asks SCTP program affected beneficiaries to explore opportunities in CDF

Salima District Commissioner Thokozile Munthali Chingeni has urged beneficiaries who will be disenrolled from the Social Cash Transfer Program (SCTP) to explore other opportunities in Reformed Constituency Development Fund (CDF).

She made the call Wednesday, when officials from the ministry of Gender announced reforms in the SCTP following about a 50 percent donation cut.

In his presentation Chief Gender Officer in the Ministry of Gender, Community Development and Social Welfare Anastazio Matewere said funding to social protection is expected to decline by more than half by January 2027.

He said this has triggered the reforms which include the government increasing its allocation from K4.8 billion to K7 billion and reducing the number of beneficiaries by 71 percent while increasing the beneficiaries' money from K16,850 to K32,040 per household.

Matewere added that the reformed CDF will target households headed by the elderly, persons with disability, children and people with chronic illness.

In an interview Chingeni said members from disenrolled households have an opportunity to join groups to access CDF women and youth loans to transform their livelihoods.

She said CDF also has a provision of bursary which will play a critical role of supporting education for underprivileged learners, noting out of K900 million, the district has received K450 million, translating to K75 million for each of the six constituencies in Salima.

The DC added that the CDF also provides an opportunity for sports development, creative arts and innovation inline with Mw2063 agenda, which affected household members can also benefit from.

“As a district will make sure to support those affected through the CDF and other programs. We will also ensure that those remaining in the program are eligible ones,” she said.

Salima District Council chairperson Fazili Adams said wars and natural calamities have affected donor support recently, urging communities to remain mindful always.

Khonsolo ya Salima yapereka zitukuko zitatu zomwe zinasankhidwa pansi pa thumba la ndalama la 5 billion Constituency Dev...
23/09/2026

Khonsolo ya Salima yapereka zitukuko zitatu zomwe zinasankhidwa pansi pa thumba la ndalama la 5 billion Constituency Development Fund (CDF) kwama kontirakitala kuti ayambe kumanga ku dera la phungu wanyumba yamalamulo ku m'mwera kwa boma la Salima.

Zitukukozi ndi monga Nyumba ziwiri za apolisi ku Ngodzi, chimbudzi chimodzi, kukonza ngalande yamadzi, kuyika zipangizo zamadzi aukhondo komanso zina, zomwe zimangidwe ndi ndalama zoposa 413 million.

Pa Chipoka Health Center nyumba ziwiri zikonzedwanso (rehabilitation) pamodzi ndi zimbudzi ziwiri, kuphatikizapo kukhonza zipangizo za madzi aukhondo ndi ndalama zoposa 458 million.

Ntchito Ina ndiyomanga nkhokwe yosungiramo mbewu yomwe imangidwe ndi ndalama zoposera 221 million kwacha.

Chitukuko chilichonse chikuyembekezereka kugwiridwa kwamasiku okwana 90.

Poyankhulapo lachitatu, phungu wakuderaku Madalitso Mazombwe walimbikitsa makontirakitala kuti amange zinthu zolimba komanso wachenjeza akomiti ndi anthu akudera kuti apewe mchitidwe wakuba ponena kuti zimabwezeretsa chitukuko mmbuyo.

Mlangizi owona zakusasiyana pakati pa amayi ndi abambo, anyamata ndi atsikana Friness Samaliya, wati anthu ogwira ntchito pamalopa akaneneze nkhanza za mtundu uliwonse komanso makontirakitala awonetsetse kuti azimayi alembedwaso ntchito.

Wothandizira mkulu owona zolemba anthu ntchito Joseph Kachigamba wauza makontirakitala kutsatira malamulo apantchito polemba anthu ntchito komanso malipiro awo.

Kudzera mu CDF palibe angadzaloze chala President Mutharika mu 2030 pa nkhani ya chitukuko - yatero nduna  Wachiwiri kwa...
23/09/2026

Kudzera mu CDF palibe angadzaloze chala President Mutharika mu 2030 pa nkhani ya chitukuko - yatero nduna



Wachiwiri kwa nduna yazaumoyo Charles Chilambula wauza anthu a m’boma la Salima kuti asankhe zitukuko za ku mtima kwawo kudzera mu K5 billion ya Reformed Constituency Development Fund (CDF).



Ndunayi yalankhula izi pamene idayendera m’mene ntchito yakatemela wa Chikuku yayambira m’bomali, pomwe anthu aku Mtauchila m’dera la mfumu yayikulu Pempa adapempha chituko chachipatala kuchoka ku Boma, kudzera kwa ndunayi.



Apa ndunanayi idati kudzera mu thumba lachitukuko latsopano la CDF President wa dziko lino Arthur Peter Mutharika adapereka mphanvu kwa anthu akumudzi kuti adzidzisankhire okha chitukuko chakumtima kwawo.



Iyo idafotokoza kuti izi zikutanthauza kuti ntchito yomanga masukulu, zipatala ndi zina, tsopano ili m’manja mwa anthu eni ake, ndipo ngati boma lingamange zitukuko zamtundu umenewu ndekuti zitha kudzera kwa mabungwe kapana maiko ena.



“Ndalama imeneyi ndiyochula kwambiri, ndipo tikayigwiritsa bwino ntchito madera athu atukukuka kwabiri,” idatero ndunayi.



Ndunayi idapereka chitsanzo cha kwawo ku Likoma komwe anthu asankha kumanga chipatala chachikula m’bomalo (District Hospital), ponena kuti boma la Likoma ndilokhalo lomwe lidalibe chipatala cha mtundu otere m’dziko muno.



Pakali pano ndunayi yati yasangalala ndi m’mene nchito yogawa katemera wachikuku yayambira ku Salima ndipo yamema makolo kuti awonetsetse kuti ana awo alandira katemerayu.



Ndunayi idafotokozanso kuti Boma likuyesetsa kuti anthu asakhale ndi njala mdziko muno polingalilanso chiwophyezo cha ng’amba chomwe chilipo.



Mfumu yayikulu Pemba idapempha ndunayi kuti Boma lithandizepo pa nkhani yanjalayi ponena kuti anthu sadakolore bwino chaka chathachi chifukwa cha ng’amba komanso adakhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi komwe kudachitika mu August chaka cha 2026.

22/09/2026

Maphunziro othandiza kuzindikira ana omwe ali ndi mavutu pamaphunziro, monga kusamva kapena kuwona bwino akuchitika m'boma la Salima ndi thandizo la Boma Iceland kudzera ku UNICEF.

Maphunzirowa, omwe ndi amasiku awiri, akukhudza aphunzitsi a sukulu zosiyana siyana m'bomali, omwe akuyembekezereka kukaperekanso ukudaulowu kwa anzawo.

Anthu osiyanasiya asonkhana pa bwalo la zamasewero la Malawi Mangoes mboma la Salima  pomwe masewero apira wa miyendo pa...
19/09/2026

Anthu osiyanasiya asonkhana pa bwalo la zamasewero la Malawi Mangoes mboma la Salima pomwe masewero apira wa miyendo pakati pa timu ya LUANAR Socials ndi ya Khonsolo ya Salima ayamba ndipo ukatha, kuseweredwa wamanja.

Mkulu wazamasewero m'boma la Salima Grace Thera Chirambo walimbikitsa ogwira ntchito pa khonsolo ya Salima kuti azikhala...
17/09/2026

Mkulu wazamasewero m'boma la Salima Grace Thera Chirambo walimbikitsa ogwira ntchito pa khonsolo ya Salima kuti azikhala ndi nthawi yopanga nawo masewero osiyanasiyana.

Iye wayankhula izi lachinayi pomwe khonsolo ya Salima ikukonzekera masewero omwe akhalepo loweruka mbomali pakati pa agwira ntchito pakhonsoloyi ndi LUANAR.

Thera wati masewero ndiwofunika chifukwa amathandizira kulimbitsa thupi komanso kulimbitsa ubale pakati pa adindo osiyanasiyana.

"Kuyenda ndikuvina ndipo anthu timayenera tizicheza bwino chifukwa opulumutsa mnzake sadziwika", Chirambo watero.

Iye wayamikiranso boma, Kampani ya M and B komanso First Capital Bank kamba kopereka thandizo monga ndalama ku masewero osiyanasiyana monga Aerobics, mpira wamiyendo, mpira wamanja komanso kuthamanga zomwe zikuthandizira kuti bomali lizichita bwino pamasewero.

Khonsolo ya Salima yamaliza kuchititsa maphunziro komanso kupereka ma satifiketu kwa anthu okwana 18 omwe anatengedwa ku...
17/09/2026

Khonsolo ya Salima yamaliza kuchititsa maphunziro komanso kupereka ma satifiketu kwa anthu okwana 18 omwe anatengedwa kuti akayendetse thumba la ndalama la Constituency Development Fund (CDF) mboma la Salima.

Poyankhula atamaliza kuchititsa maphunzirowa lachitatu, DC waboma la Salima Thokozile Munthali Chingeni wati cholinga chamaphunzirowa kunali kufuna kupereka ndondomeko zoyenera zakagwiritsidwe ntchito ka thumba la ndalama la CDF.

Chingeni wati anaitanaso bungwe lothana ndi ziphuphu ndi katangale kuti akaphunzitse anthuwa momwe angapewere katangale pamalo ogwirira ntchito.

Iye walimbikitsa anthuwa kukaneneza aliyense opanga chinyengo ponena kuti palibe amene amasewera ndi ndalama zaboma.

Mkulu wowona za anthu ogwira ntchito Dallys Mkaka walimbikitsa anthuwa kukafika malo ogwirira ntchito nthawi yabwino, kupereka uthenga wa momwe ndalama zagwirira ntchiti, kusunga chinsinsi komanso kugwira ntchito bwino ndi anthu akudera mosakondera.

Mmodzi mwa othandizira kusunga chuma ku thumba la CDF, Elias Mjima wayamikira khonsolo ya Salima kamba kamaphunzirowa ponena kuti athandizira kulumikizana kwabwino pakati pawo zomwe zithandizire kukhalaso ndi ubale wabwino ndi anthu akudela.

DC wa Boma la Salima Thokozile Munthali Chingeni wayamikira komiti yowona za malonda a zakudya ndi zakumwa pa ntchito yo...
17/09/2026

DC wa Boma la Salima Thokozile Munthali Chingeni wayamikira komiti yowona za malonda a zakudya ndi zakumwa pa ntchito yowonetsetsa kuti ukhondo ukutsatidwa pa bizinesi kuti ogula atetezedwe.

Iye wati ndipofunika kuti anthu abizinesi amvetsetse kuti ntchitoyi siyitanthauza kudana nawo anthu a bizinesiwa koma kuteteza ogula kuzinthu zomwe zingayike miyoyo yawo pachiswe.

Wapampando wa komitiyi a Jason Adam afotokoza kuti posachedwapa komitiyi yatseka malo awiri omwera mowa omwe awuzidwa kuti akonzeso nyumba zawo za malonda popeza zimayika miyoyo ya anthu pachiswe.

Iye wati komitiyi idauzanso amalonda ena kuti akonze zithu zina monga kuyika ma toilet komanso madzi osamba m'manaja kuti khonsolo ithe kuwapatsa zikalata zochitira malonda.

Iye wafotokozanso kuti komitiyi idachotsanso nyama yowonongeka yolemera pafupi fupi 71kgs pa msika, ndikuyiwotcha.

Jason wati komitiyi ipitiriza kugwira ntchito yoyendera ma bizinesiwa kuphatikizapo malo odyera kapena kuti ma restaurant.

Address

Salima

Opening Hours

Monday 07:30 - 17:00
Tuesday 07:30 - 17:00
Wednesday 07:30 - 17:00
Thursday 07:30 - 17:00
Friday 07:30 - 17:00

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Salima District Council posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share