29/07/2026
Tikupitiliza ntchito yoonesesa kuti wina aliyense akutsatia malamulo pa nkhani ya bizinesi ya kabaza mu mzinda wa Mzuzu.
Zomwe tikulimbikitsa n**i:
1. Kabaza asayendetse mu mseu wa ukulu wa M1 komanso mu Orton Chirwa Avenue.
- Apa ndiye kuti mseu ochoka pa Katoto roundabout mpaka Luwinga ndiwoletsedwa.
-Mseu ochoka pa katoto roundabout - Highway - Mzuzu Court House ndioletsedwa.
2. A Kabaza omwe akulowa mkati mwa town akhale ndi zonse zowayeneleza kuphatikizapo certificate yoti anachita nawo maphunziro apamseu.
3. Njinga ya moto yikhale ndi zonse zoziyeneleza kuyenda pa mseu monga number plate, zipewa ziwiri, mwa zina.
4. Wina aliyense azichikela muma rank obvomelezeka osati kuyima paliponse.
Wina akapezeka kuti sakutsatila izi, tikumamugwira, kumulanda njinga ndipo amayenela kuti alipire K50000 njinga yakapalasa ndi K70000 njinga ya moto.
Zonsezi zikuchitika ngati mbali imodzi yochepesa ngozi, kupulumusa miyoyo komanso kulimbikitsa chitetezo
Kabaza ndiofunika kwambiri pachitukuko cha mzinda wathu komano pakufunika titsatile malamulo kuti chisakhale chiphinjo kwa ena..
Mzuzu wanga
Mzinda wanga
Msumba wane
Udindo wanga!