12/09/2026
Chawezi Banda writes:
KUKAMACHA MUPEZA NKHANI IYI
Nthawi zambiri ndikakhala pa TV ndinkanena kuti, boma la Chakwera lapanga zinthu zambiri koma silitha kuyankhula kuti anthu azidziwa zimene likuwapangira.
Mwaiona nyuzi iyi?
Akuti pamene Blantyre Water Board inkakumana ndi mavuto, boma la a Chakwera mwakachetechete linaombola kampaniyi ndi MK24 billion polipira ku ESCOM kuti madzi asakhale vuto anthu mudzikhala mofatsa mtima uli pansi.
Izizi zinathandizira kuti chuma cha bungweli chidziyenda bwino komanso ntchito zake zinapita patsogolo.
Ndiye mudzidabwa kuti madzi nthawi ya Chakwera samavuta? Leadership gentlemen. Leadership yopanda phokoso koma zinthu pa ground nkumatheka.
Lero ESCOM m'dziko loti tili ndi president, ma vice ake awiri yafika polemba kalata kuti idula magetsi ku Blantyre Water Board onsewa angoyang'anira. Madzi akuvuta. Magetsi akuvuta.
Ndiochepa amene amamvetsa tikamati Chakwera uja anatsogolera boma limene limadziwa ndikumvetsa udindo wake pa anthu amene analisankha.
Pano ntchito zake zikumuyankhulira angakhale ali kunja kwa boma.