25/01/2021
41. (lye) adati: "Mbuye wanga! Ndipatseni Chizindikiro!" Adati: "Chizindikiro chako Ndikuti sudzatha kulankhula ndi anthu mpaka Masiku atatu koma momangolozera (ndi Chala) basi. Ndipo tamanda Mbuye wako, Kutamanda kwambiri ndiponso Umlemekeze (popemphera) madzulo Ndi m'mawa".
42. Ndipo (kumbukira) pamene angelo adati: "E Iwe Mariam! Ndithudi, Mulungu Wakusankha, Wakuyeretsa ndipo Wakulemekeza, mwa Akazi onse amitundu ya anthu".
🅝🅓🅔🅜🅐🅝🅖🅐
Apa patchulidwa nkhani ya mayi Mariam (Maria) pomwe adatha msinkhu ndi pomwe mngelo adamuuza nkhani yabwinoyi.
43. "E iwe Mariam, dzichepetse Kwa Mbuye wako ndi Kumlambira powerama pamodzi Ndi owerama".
44. Izi ndizina mwankhani zobisika zomwe Tikukuvumbulutsira. Sudali nawo pamene Amaponya zolembera zawo (m'madzi m'njira Ya mayere) kuti aone ndani mwaiwo alere Mariam. Sudali nawo pamene adali kutsutsana.
45. (Kumbukira) pamene mngelo adati: "E iwe Mariam (Maria)! Mulungu akukuuza nkhani Yabwino (kuti ubereka mwana popanda Mwamuna Koma kupyolera mu) liwu lochokera Kwa lye (Mulungu, lakuti, "Bereka," ndipo Nkubereka Popanda kupezana ndi mwamuna). Dzina lake ndi Mesiya Yesu mwana wa Mariya, adzakhala wolemekezeka padziko lapansi ndi pa Tsiku lachimaliziro; ndiponso ndi mmodzi wa Oyandikitsidwa kwa Mulungu.
46. "lye adzayankhula ndi anthu Ali mchikuta ndi kuukulu (Wake). Ndipo adzakhala Mmodzi wa anthu abwino".
47. (Mariam) adati: "Mbuye wanga! Ndingakhale ndi mwana Bwanji pomwe sadandikhudze Munthu aliyense (mwamuna)?" (Mngelo) adati: "Ndi Momwemo. Mulungu Amalenga chimene wafuna. Akafuna chinthu amachiuza: "Chitika," ndipo chimachitikadi.
48. Ndipo Mulungu adzamphunzitsa Kulemba, nzeru, Taurat ndi Injili.
49. "Ndipo (adzamchita kukhala) Mneneri Kwa ana a Israeli (adzakhala akuwauza kuti): "Ine ndakudzerani ndizizindikiro kuchokera Kwa Mbuye wanu kuti ndikuumbireni dongo Ngati chithunzi chambalame, nkuuzira M'menemo nkukhaladi mbalame Mwachilolezo cha Mulungu; Ndipo ndichiritsa osapenya chibadwire, Ndiwamangamaanga, ndi kuukitsa wakufa Mwa chilolezo cha Mulungu; ndipo ndikuuzani Zomwe mudye ndi zimene musunge m'nyumba Zanu.Ndithudi, m'zimenezi muli zizindikiro Kwa inu ngati mulidi anthu okhulupirira.
🅝🅓🅔🅜🅐🅝🅖🅐
Apa akunena zina mwazozizwitsa zomwe Mneneri Isa (Yesu) anadza nazo. Ndipo zina mwaizo ndikuumba ndidongo chifanizo chambalame. Kenako nkuchiuzira chikhaladi mbalame yamoyo mwachilolezo cha Mulungu.
°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°
50. "Ndipo (ndikhala) wotsimikizira zomwe Zidalipo patsogolo panga (m'Buku la) Taurat. Ndipo ndadza kuti ndikulolezeni Zina mwa zomwe zidaletsedwa kwa inu. Ndipo ndakudzerani ndi zizindikiro Kuchokera kwa Mbuye wanu (zotsimikizira Uthenga wanga). Choncho, opani Mulungu ndi kundimvera (ine).
51. "Ndithu Mulungu ndiye Mbuye wanga ndiponso Mbuye Wanu; choncho mupembedzeni. Iyi ndiyo njira yoongoka".
52. Koma pamene Yesu adazindikira mwa iwo Kusakhulupirira adati: "Ndani akhale athandizi Anga kwa Mulungu (popitiriza kufalitsa Chipembedzo Chake)?" Ophunzira ake Adati: "Ife ndife athandizi a Mulungu (pofalitsa Chipembedzo Chake). Takhulupirira Mulungu; ndipo ikira umboni kuti ife ndithu Ndi odzipereka (kwa Mulungu).
53. "Mbuye wathu! Tazikhulupirira Zimene mwavumbulutsa, Ndipo tamtsata Mtumikiyo. Choncho tilembeni pamodzi Ndi oikira umboniwo."
54. Ndipo (Ayuda) adakonza chiwembu (chofuna Kupha Yesu) Mulungu adachiwononga Chiwembu chawocho. Mulungu ngokhoza bwino zedi Poononga ziwembu za anthu a chiwembu.
55. (Kumbukirani) pamene Mulungu adati: "Iwe Yesu! Ine ndikukwaniritsira nyengo yako Yokhala ndi moyo. (Ayuda sachita kanthu Kwa iwe). Ndipo ndikunyamulira kwa Ine Ndikuyeretsa kwa anthu osakhulupirira (omwe Ndi adani ako). Ndipo amene akutsata (Iwe) Ndiwasankha kukhala apamwamba pa amene Sadakhulupirire kufikira tsiku lachimaliziro. Kenako kobwerera kwanu nkwa Ine, ndipo Ndidzaweruza pakati panu pazomwe mudali Kusiyana.
56. Tsono amene sadakhulupirire, Ndiwakhaulitsa ndi chilango chaukali padziko lapansi ndi tsiku lomaliza, ndipo Sadzapeza athandizi.
57. Koma amene akhulupirira Nachita zabwino, (Mulungu) adzawalipira malipiro Awo (mokwanira). Ndipo Mulungu Sakonda anthu ochita zoipa.
58. Izi tikukuwerengera iwezi Ndi zivumbulutso ndi ulaliki waluntha.
59. Ndithudi, fanizo la Yesu kwa Mulungu lili ngati fanizo la Adam; adamulenga ndi dothi namuuza kuti: "Khala munthu," Ndipo adakhaladi.
🅝🅓🅔🅜🅐🅝🅖🅐
(Ndime 59-62) Ndime iyi idavumbulutsidwa pamene nthumwi za chikhirisitu zidadza kwa mtumlki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) kuchokera ku Najirani. Iwowo adakangana ndi Mtumiki wa Mulungu pa nkhani ya Yesu. Iwo adati kwa Mtumiki wa Mulungu "Bwanji iwe ukutukwana Mneneri wathu?" lye adati: "Kodi ndikutukwana chotani?" Iwo adati: "Iwe ukuti iyeyo ndikapolo wa Mulungu." lye adati: "Inde. lyeyo ndi kapolo wa Mulungu ndiponso mawu ake omwe adawaponya mwanamwali." Zitatero iwo adapsa mtima ndipo anakwiya nati, "Kodi iwe udamuonapo munthu wobadwa popanda tate? Ngati ukunenadi zoona tationetsa munthu wotere." Apa mpomwe Mulungu adavumbulutsa ndime yakuti "Ndithudi, fanizo la Yesu (Isa) kwa Mulungu lili ngati fanizo la Adam". Kenako anawaitanira ku Chisilamu. Iwo adati: "Tidalowa kale m'Chisilamu iwe usanadze." Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) adati: "Mwanama. Pali zinthu zitatu zikukuletsani kulowa m'Chisilamu: (a) Kunena kwanu mawu oti Mulungu wadzipangira mwana. (b) Kudya kwanu nyama ya nkhumba. (c) Kulambira kwanu mtanda." Pamene adapitiriza kumtsutsa Mneneri Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale naye) adawapempha kuti atembererane ponena kuti, "O! Ambuye Mulungu! Mtemberereni ndi kumlanga amene akunena zabodza mwaife pankhani ya Yesu! Pompo Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) adasonkhanitsa anthu ake. Koma iwo atakhala upo adagwirizana kuti asalole kuopa kuti chilango chingawatsikire. Potero zidadziwika kwa anthu kuti iwo ngabodza.
°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°°
60. (Ichi ndi) choona chochokera Kwa Mbuye wako; choncho Usakhale mwaokaikira.