Mchinji District Council

Mchinji District Council This is the only official page for Mchinji District Council for all developments, updates, functions happening in Mchinji

The only official page for Mchinji District Council

Linali tsiku la chisoni kwambiri pamene thupi la malemu Traditional Authority ( TA) Mponda, limalowa mmanda lero lachiwi...
04/08/2026

Linali tsiku la chisoni kwambiri pamene thupi la malemu Traditional Authority ( TA) Mponda, limalowa mmanda lero lachiwiri ku likulu kwawo la Kanyenje.

Malemu TA Mponda anamwalira loweruka kuchipatala cha boma cha Mchinji atadwala kanthawi kochepa.

Mkulu oyang'anira mafumu ku unduna wa maboma aang'ono a Charles Makanga anali nawo pa mwambo woyika mmanda malemu mfumuyi ndipo anati malemuwa anali odziwa kuthetsa mikangano komanso amadziwa zambiri za zitukuko.

A Makanga anapempha a ku banja kuti apewe mikangano pamene akusankha mlowammalo wa malemuwa.

A ku banja asankha a Alines Makaniko kuti alowe mmalo mwa mfumu yatisiyayi.

Anthu ochuluka kuphatikiza mafumu a chiChewa, akuluakulu a khonsolo komanso anthu a kuderali anaperekeza malemu wa.

Malemu TA Mponda asiya mkazi ndi ana asanu ndi anayi.

Zotsatira za momwe ma khonsolo achitira bwino kapena ayi pa kagwiridwe zotchedwa Local Authority Assessment (LAPA) zaper...
31/07/2026

Zotsatira za momwe ma khonsolo achitira bwino kapena ayi pa kagwiridwe zotchedwa Local Authority Assessment (LAPA) zaperekedwa mu mzinda wa Lilongwe.

Zotsatira ndi zomwe zimapangitsa kuti khonsolo ilandire ndalama zija za Governance to Enable Service Delivery (GESD) komanso Regional Climate Resilience Programme (RCRP).

Khonsolo yanu ya Mchinji yachita bwino ndipo yapeza nawo mwayi olandira ndalama za chitukuko za GESD komanso za RCRP.

Khonsolo yi ili pa nambala 15 pa ma khonsolo 28.

Ndalama zomwe khonsolo yapatsidwa ndi K1.2 billion ya GESD komasno K607 million za RCRP 2.

Zotsatira za ma interview a ma constituency assistant accountant, constituency assistant procurement officer, and consti...
14/07/2026

Zotsatira za ma interview a ma constituency assistant accountant, constituency assistant procurement officer, and constituency works supervisor za Mchinji.

06/07/2026
SHORTLISTED CANDIDATES FOR THE POST OF TEMPORARY REGISTRATION ASSISTANTS Mchinji District Council would like to invite s...
03/06/2026

SHORTLISTED CANDIDATES FOR THE POST OF TEMPORARY REGISTRATION ASSISTANTS

Mchinji District Council would like to invite shortlisted candidates for the post
of Temporary Registration Assistant to attend written interviews which have been
scheduled as follows:

VENUE: Mchinji Teachers Training College
DATE : 5th June, 2026 (Friday)
TIME : 7:30 AM

NOTE: All the candidates are requested to bring original ceftificates, National
Identity Card, and writing materials.

Khonsolo ya Mchinji lero ikukhazikitsa lamulo lomwe mtsogoleri wa dziko lino anakhazikitsa losamalira malo ndi ukhondo m...
28/05/2026

Khonsolo ya Mchinji lero ikukhazikitsa lamulo lomwe mtsogoleri wa dziko lino anakhazikitsa losamalira malo ndi ukhondo mmalo omwe akukhala komanso kuchitira malonda.

Mwambowu ukuchitikira ku Kapiri komwe khonsoloyi motsogozedwa ndi bwanankubwa Reinghard Chavula, akusesa mu msika komanso malo ozungulira Trading Centre yi.

Mfumu yaikulu Dambe, wapampando wa khonsolo a Kennedy Chipanga, wamkulu wa polisi a Dr David Kumwenda, akuluakulu a za umoyo, ochita malonda, akuluakulu a mabungwe omwe si aboma, akulu akulu a banki ya Centenary, ogwira ntchito mu boma komanso achinyamata anatenga nawo gawo.

Prof. Arthur Peter Mutharika, anayika lamulo loti malo onse aboma, okwerera mabasi, misika, ndi malo ogwirira ntchito akhale ndi zida zothandizira ukhondo. Cholinga cha lamuloli ndi kuteteza anthu ku matenda monga kolera.

Mwachidule, lamulo li likuti malo aboma ndi misika, malo okwerera mabasi, malo oyima galimoto (car parks), ndi malo ena onse okhala anthu ambiri ayenera kukhala ndi malo abwino otayira zinyalala komanso malo ogwirira ntchito ndi masukulu aboma ndi a private komanso malo ogwirira ntchito ayenera kukhala ndi zida zothandizira ukhondo ndi zotayira zinyalala.

Ma khonsolo ndiponso ma bungwe azaumoyo ayenera kuonetsetsa kuti lamuloli likuyenda.

Achinyamata amakhala otakataka...Achinyamata youth network ya kwa Zulu mmawa wa pa 14 May anali kalikiliki kusesa ndi ku...
14/05/2026

Achinyamata amakhala otakataka...Achinyamata youth network ya kwa Zulu mmawa wa pa 14 May anali kalikiliki kusesa ndi kukonza ku chipatala chachikulu cha Mchinji.

Mogwirizana ndi Space4Youth and Zikomo Social Net achinyamata a Zulu Youth Network wa agwira ntchito yotamandika pofuna kuonesetsa kuti ka chipatala kwathu kuli ukhondo.

Mkulu oyang'anira achinyamata ku Mchinji a Ian Sukali ayamikira achinyamata wa ponena kuti izizi zikuonetaeratu poyera kusintha kwa kaganizidwe pamene achinyamata akuyikidwa patsogolo molunjika Malawi 2063.

Zulu Youth Network
Zikomo Social Net
Space4Youth Business Hub

Happy Kamuzu Day...14th May!
14/05/2026

Happy Kamuzu Day...14th May!

Mu nkhani zina.... Banki ya Centenary yathandiza khonsolo ya Mchinji ndi zipangizo zogwiritsa ntchito posamalira malo os...
08/05/2026

Mu nkhani zina.... Banki ya Centenary yathandiza khonsolo ya Mchinji ndi zipangizo zogwiritsa ntchito posamalira malo osiyansiyana.

Happy Labour Day!
01/05/2026

Happy Labour Day!

Address

McHinji

Telephone

+2651242111

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mchinji District Council posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Organization

Send a message to Mchinji District Council:

Shortcuts

Share