10/08/2026
BUNGWE LA LAW COMMISSION LAYAMBA KUMVA MAGANIZO A ANTHU MU NDONDOMEKO YOUNIKA MALAMULO OLETSA MCHITIDWE OKWATITSA ANA
Bungwe la Law Commission lero layamba ntchito yofunsa ndi kumva maganizo m’madera osiyanasiyana m’dziko muno pa ntchito yokonza lamulo lolimbana ndi mchitidwe okwatitsa ana komanso kuteteza ana amene ali kale m’maukwati.
Kufunsa maganizoku kukuyendetsedwa ndi komiti ya akatswiri yomwe ili ndi nthumwi zochokera m’madipatimenti ndi maunduna monga unduna wa zachilungamo, unduna woona kuti pasakhale kusiyana pakati pa amai ndi abambo ndi ana, unduna wa zachuma, nthambi za polisi komanso mabungwe omwe si aboma.
Wachiwiri kwa mkulu Woyang’anira za Kusintha Malamulo ku Law Commission, a Robert Kandulu, wati kufunsa maganizoku ndi mbali imodzi ya ntchito za Bungweli pomwe limayenereka kusonkhanitsa maganizo oyambilira kuchokera kwa anthu ndi mabungwe osiyanasiyana kuti zithandize pokonza lamulo lomwe likukonzedwa.
A Kandulu ati ntchitoyi ikuchitika mogwirizana ndi gawo 7 la Lamulo la Law Commission Act, lomwe limapatsa Bungweli mphamvu zokambirana ndi kufunsa maganizo kwa anthu ndi adindo mdziko lonse.
“Izi zikuchitika mogwirizana ndi zomwe zili mu Ndime 7 ya Lamulo la Law Commission, yomwe imalola Bungweli kufunsa maganizo ndi kufotokoza mfundo zoyambilira pa ntchito yowunika kapena kukonza lamulo,” anafotokoza a Kandulu.
Kufunsa maganizoku kukuchitika m’zigawo zonse za dziko la Malawi, pomwe mamembala a komiti ya akatswiriyi akukumana ndi anthu komanso adindo osiyanasiyana.
Lero, mamembala a komitiyi akuchita zokambirana ku Rumphi, Nsanje, Dedza ndi Mangochi, kumene akuyembekezeka, mwa zina,] kusonkhanitsa maganizo, kumva zomwe anthu akukumana nazo pantchito yoletsa mchitidwe okwatitsa ana, mavuto a maukwati a ana komanso mfundo zomwe zingatsatidwe pofuna kuteteza ana amene ali kale m’maukwati.
Zomwe zisonkhanitsidwe kudzera m’kufunsa maganizoku zithandiza pokonza malamulo omwe cholinga chake ndi kulimbikitsa chitetezo cha ana komanso kuthana ndi mchitidwe okwatitsa ana m’dziko la Malawi.