02/06/2026
Mkulu wa Apolisi achereza Kazembe wamkulu wa dziko la Britain
Mkulu wa Apolisi m'dziko muno, bambo Richard Chakupaleza Chikoko Luhanga, pa 2 June 2026 analandira mayi Leigh Stubblefield, Kazembe wamkulu wa dziko la Britain ku Malawi, pa ulendo wa ulemu ku likulu la Apolisi ku Area 30, ku Lilongwe.
Ulendowu ndi gawo la maubwenzi ndi zokambirana zomwe a Luhanga akuchita nthawi ndi nthawi ndi mabungwe komanso anthu omwe ali ndi chidwi pa ntchito za Apolisi komanso chitetezo cha anthu m'dziko muno.
Pa mkumano wu, akuluakulu awiriwa anakambirana nkhani zosiyanasiyana zomwe zikukhudza njira zolimbikitsira mgwirizano pothandiza ntchito za Apolisi.
A Luhanga anayamikira a Stubblefield chifukwa cha ulendowu ndipo atsimikiziranso kudzipereka kwa Apolisi posunga maubwenzi abwino omwe amathandiza Apolisi kugwira ntchito mwa ukadaulo.
Superintendent Alfred Chimthere
Wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za Apolisi m'dziko muno