03/10/2026
DPP YALEPHERA
Wapampando wa msika wa Ngabu ku Chikwawa, Austin Bvumbe wati muchaka chimodzi chomwe chipani Cha DPP chakhala chikulamulira dziko lino, zachuma sizikuyenda bwino.
Bvumbe wati mu ulamuliro wa chipani Cha MCP, anthu amakwanitsa kupanga business ndikupaga phindu koma ulamuliro wa chipani cha DPP motsengozedwa ndi a Peter Muntharika walephera muchaka choyamba Cha ulamuliro wake.
" Chitengeleni boma pa 16 September 2025 kuzafika lero, zinthu zasokonekera. Tikakamba zama businesse, anthu poyamba amakwanitsa kumanga nyumba, amakwanitsa kumanga shop mumsika koma lero anthu akungulitsa ma shop komanso nyumba kusonyeza kuti utsogoleri wa a Peter Muntharika palibe chilichonse chimene chikuendapo iyayi" atelo Bvumbe.
Koma masiku apitawa nduna yazachuma Joseph Mwanamvekha anati chuma chikuyenda bwino dziko muno.