16/06/2026
Mtsogoleri wa Zipani Zotsutsa M’nyumba ya Malamulo, a Simplex Chithyola Banda, wadzudzula boma chifukwa cholephera kuthana ndi mavuto a m’dziko muno moyenera, kuphatikizapo masautso omwe aMalawi omwe ali ku South Africa akukumana nawo komanso kukwera kwa mavuto azachuma.
M’chikalata chomwe atulutsa lero, a Banda apempha boma kuti lichitepo kanthu mwachangu pofuna kuthandiza nzika zomwe zili m’masautsozi.
Pa zogawanitsa Mtundu, iwo adzudzula zomwe adalankhula Nduna yowona ubale ndi maiko ena, a George Chaponda, zokhudza a Malawi amtundu wa Chingoni aku Mzimba, ndipo achenjeza kuti malankhulidwe oterewa akhoza kusokoneza mgwirizano ndi mtendere wa dziko.
A Banda awonetsa kukhudzidwa mtima kwambiri ndi zomwe zikuwoneka ngati njira zofuna kufooketsa komanso kuchepetsa ulamuliro wa Ofesi ya Wachiwiri kwa Purezidenti wa dziko lino.
Iwonso adzudzula kukwera kwa mchitidwe wosalolerana pa ndale, kugwiritsa ntchito molakwika mabungwe a boma, komanso mchitidwe wachibale (nepotism) pa ntchito za boma.
A Banda apempha atsogoleri a boma kuti aziyika patsogolo kukhala odalirika komanso owonekera poyera (accountability), ndikukhazikitsa ndondomeko zomwe zikuthandiza nzika poyamba, makamaka pa nthawi yomwe mitengo ya Katundu komanso kusowa kwa ntchito (ulova) zikukwera m'dziko muno.