19/03/2026
DPP RSA WING
Nduna ya Zachidziwitso ndi Ukadaulo wa Mauthenga (ICT), a Dr. Shadric Namalomba, lero akuchita msonkhano wogwira ntchito ku likulu la Malawi Communications Regulatory Authority (MACRA) ku Blantyre.
Ulendowu ukubwera potsatira malangizo a Purezidenti a Peter Mutharika amene anapereka pa State of the Nation Address posachedwapa, pomwe anauza mabungwe onse a boma kuti ayambe kugwiritsa ntchito ukadaulo wa pa digito (digitalisation) pa ntchito zawo.
Pa msonkhanowu, a Namalomba akufuna kuona mmene MACRA limodzi ndi madipatimenti ena omwe ali pansi pa unduna wake akukonzekera kutsatira malangizo a Purezidenti, pofuna kuonetsetsa kuti ntchito za boma zikuyenda mwachangu, mwachilungamo komanso mogwiritsa ntchito ukadaulo wamakono.
Kuphatikiza apo, Ndunayi akuyembekezeka kulimbikitsa kugwiritsa ntchito ma system a pa intaneti pa ntchito za boma, kupititsa patsogolo kulumikizana (connectivity) mdziko muno, komanso kulimbikitsa chitetezo cha pa intaneti (cybersecurity) kuti deta ya boma ndi ya nzika zitetezeke.
Iye ananenanso kuti kusintha kupita ku digitalisation kudzatsegula mwayi kwa achinyamata, kulimbikitsa bizinesi za pa intaneti, komanso kuthandiza kuti ntchito za boma zizipezeka mosavuta kwa nzika zonse za Malawi, ngakhale kumadera akumidzi.
Boma likukhulupirira kuti njira imeneyi ithandiza kuchepetsa ziphuphu, kusunga nthawi, komanso kupititsa patsogolo chitukuko cha dziko.
Democratic Progressive Party - DPP Stella Salima WaBobi Mwiza Kays Nkhonjera Mike Mike Nyirenda Stengie Gaster Tshabalala Akefe Kufa Mviza