23/04/2026
LIFE IS A LONG JOURNEY
PART 1
CHONDE MUSANAYAMBE KUWELENGA NKHANIYI TIPANGENI FOLLOW Nyamata wa ntopola PGS KUTI MA PART OTSATILA MUWAPEZE MOSAVUTA NDIPO PANGANI SHARE KU MA GROUP NDI ANZANU OMWE AMAKONDA NKHANI NAWO AYITSATE NAWO OMWE MULI NAWO
Moyo ndi ulendo wautali⌠ndipo palibe amene amadziwa komwe udzamutengere.
Pa mudzi wina wotchedwa Chitedze, pafupi ndi mzinda wa Lilongwe, panali mnyamata wina dzina lake Kelvin Banda. Kelvin anali mwana wa zaka 18, wamtendere, wanzeru, koma moyo wake unali wodzaza ndi mavuto.
Ankakhala ndi amayi ake okha, dzina lake Agnes. Bambo ake anamwalira ali aangâono kwambiri, choncho moyo wonse unakhala pa mapewa a amayi ake.
Tsiku lililonse, Agnes ankadzuka m'mawa kwambiri kupita ku msika kukagulitsa tomato, masamba, ndi anyezi. Koma ndalama zimene ankapeza sizinkakwanira ngakhale kugula chakudya chokwanira.
Nthawi zina ankagona ndi njala.
Koma Kelvin⌠anali ndi loto lalikulu.
âOne day ndidzakhala successful⌠ndidzachotsa amayi anga mu umphawi, no matter what.â
Izi ankazibwereza nthawi zambiri, ngakhale moyo sunali kumumwetulira.
Moyo wa Kusukulu
Kelvin anali ku secondary school, Form 4. Anali mâmodzi mwa ophunzira abwino kwambiri pa sukulupo. Aphunzitsi ake ankakonda kwambiri chifukwa cha khama lake.
âKelvin is one of the best students we have,â anatero aphunzitsi ena tsiku lina.
Koma vuto lake linali limodziâschool fees.
Nthawi zambiri ankachotsedwa kusukulu chifukwa chosowa ndalama. Izi zinayamba kumuvuta kwambiri.
Tsiku lina, ali mkalasi akuphunzira, munthu wina anabwera kudzamupeza.
âKelvin Banda?â
âYes, sirâŚâ anayankha mwamantha.
âHead teacher akukufuna.â
Mtima wake unayamba kugunda kwambiri.
Atalowa mu office, head teacher anamuyangâana mozama.
âKelvin, you are a good student. But rules are rules. Popanda fees, you cannot continue.â
Kelvin anangokhala chete.
âGo home, and come back with fees.â
Mawuwo anamudula mtima.
Kupweteka kwa Mtima
Kelvin atatuluka kusukulu, anayenda yekha mpaka kunyumba. Sanalankhule ndi aliyense.
Atalowa mânyumba, anapeza amayi ake akuphika nsima ndi ndiwo za masamba.
âKelvin, wabwera msanga lero?â anafunsa amayi ake.
Kelvin sanayankhe nthawi yomweyo. Kenako anati mofooka:
âAmayi⌠andichotsa kusukulu.â
Amayi ake anasiya zomwe ankachita.
âChifukwa chiyani?â
âFeesâŚâ
Maso a amayi ake anayamba kudzaza ndi misozi.
âMwana wanga⌠ndakhala ndikuyesetsa, koma zinthu zikuvuta kwambiri.â
Nthawi imeneyo, Kelvin anamva ngati dziko lonse lagwa pa mapewa ake.
Koma sanalire.
Anangoti:
âItâs okay amayi⌠ndidzapeza njira.â
Chisankho Chosintha Moyo
Usiku womwewo, Kelvin sanagone.
Ankaganiza zambiriâŚ
âNgati ndikhala chonchi, sindidzafika kulikonse. Ndiyenera kuchita something.â
Mâmawa mwake, asanatuluke dzuwa, Kelvin anadzuka.
âUkupita kuti mwana wanga?â anafunsa amayi ake.
âKu town⌠ndikafune ntchito.â
Amayi ake anadabwa.
âKoma iwe ndi mwana sukuluâŚâ
Kelvin anangonena mwamphamvu:
âI need to fight for my future.â
Moyo wa Ku Town
Kelvin atafika ku town, moyo sunali wosavuta.
Anayamba kugwira ntchito yonyamula katundu ku msika. Anthu ankangomuitana:
âBoy! Bwera kuno!â
Ankanyamula matumba olemera, nthawi zina ankavutika kwambiri.
Nthawi zina anthu sankamulipira.
Nthawi zina ankachita manyazi.
Koma Kelvin sanasiye.
Tsiku lina, ali wotopa kwambiri, anakhala pansi pafupi ndi shop ina.
Munthu wina wovala bwino, ngati businessman, anamuona.
Anayandikira pafupi.
âWhatâs your name, young man?â
Kelvin anayankha mwaulemu:
âKelvin, sir.â
âWhy are you working this hard?â
Kelvin anayamba kufotokoza zonseâŚ
Za moyo wake, za sukulu, za amayi ake⌠ndi maloto ake.
Munthuyo anamuyangâana kwa nthawi yayitali, osanena chilichonse.
Kenako anati:
âHmm⌠I like your spirit.â
Kelvin anadabwa pangâono.
Munthuyo anatulutsa khadi mu pocket yake, namupatsa.
âCome see me tomorrow.â
Kelvin anayangâana khadiloâŚ
Dzinalo linali:
Mr. Richard Phiri â CEO
Mtima wake unayamba kugunda kwambiri.
âCEO??â
Anayangâana mmwamba, koma munthuyo anali atachoka kale.
Chiyambi cha Kusintha?
Kelvin anakhala pansi, akuyangâana khadilo.
âCould this be my chanceâŚ?â
Koma nthawi yomweyo, mantha anayamba kulowa.
âBwanji ngati ndi prank? Bwanji ngati zinthu zisinthe?â
Komabe, mumtima mwake munali chinthu chimodzi:
Chiyembekezo.
(To be continuedâŚ)Life is a Long Journey â Part 1

(To be continuedâŚ)
Tabwelaso tiyese nawo tili ndi group pa wapp ngati mukulifuna tihaleni pa +258862702022 or kulowa kudzela mu link ili mu coment box mu
APATSENI ANZANU AWELENGE NAWO