29/05/2026
Chiwerengero Cha maukwati a ana komaso anthu opalamula milandu kamba ka mikangano akuti chatsika tsopano mdera la Mfumu Yayikulu Mankhambira m’boma la Nkhata Bay.
Nthambi yoona za chisamaliro cha ana ku Nkhata Bay District Council yomwenso ndi gawo limodzi la Nkhata Bay Civic Education Hub, inatsindika pa zokambirana za District Executive Committee, kuti chiwelengerochi chatsika kuchoka pa maukwati anayi (4) mu chaka cha 2024 kufika pa awiri mu chaka cha 2025.
Nthambiyi yati kusinthaku kwadza kamba ka ntchito yomwe Mankhambira Civic Education Hub yomwe pa Chichewa imatchedwa kuti Pabwalo ikugwira poonetsetsa kuti anthu asinthe kaganizidwe ndi kachitidwe pa nkhani zoteteza ana komanso kulimbikitsa umodzi ndi mtendere mu derali.
European Union in Malawi Ministry of Local Government and Rural Development-Malawi NICE Public Trust Malawi Malawi Government